Bungwe la Tikondane Positive Living Support Organization (TIPOLISO) lati liwonetsetsa kuti sukulu zomwe zimayang’aniridwa ndi bungweli, zikutsatira njira zomwe boma linakhazikitsa zopewera nthenda ya Covid-19.
Mkulu wa bungweli mayi Celina Bomani anena izi ku Chipini m’boma la Zomba, pomwe amakayendera sukuluzi.
Iwo ati ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana za kapewedwe ka nthendayi kaamba koti ndi omwe amakhala ndi anawa asanapite ku sukulu.
“Makolo tikugwira nawo ntchito yotamandika powonetsetsa kuti akuphunzitsa ana awo za kapewedwe ka nthendayi monga kuvala mask akamabwera ku sukulu,” anatero mayi Boman.
Mwazina mayi Bomani ati kupatula kupereka maphunziro, bungwelinso likugwira ntchito zina monga kuteteza zachilengedwe, kuphunzitsa za ulimi wa mlera nthaka komanso kusamalira ana amasiye.
Ntchitoyi ikugwiridwa m’madera Group Village Headman Mwangata, Kapalasa, Kalaliki, Balamanja komanso Mbulukutu m’boma la Zomba.
Source: https://www.radiomaria.mw/bungwe-la-tipoliso-lapempha-makolo-ateteze-ana-ku-covid-19/